Bungwe la MACRA mothandizana ndi a Youth Net Counselling (YONECO) alangiza zakufunikira kogwirana manja poonetsetsa kuti ana ali otetezeka pamene akugwiritsa ntchito intaneti.
Izi zinakambidwa pa sukulu ya Zomba Catholic Secondary pamwambo okumbukira malo otetezeka pa intaneti padziko lonse, womwe umakumbukiridwa pa 2 February chaka chilichonse, ndipo dziko la Malawi likuchita mwambowu kuyambira pa 23 mpaka pa 25 mwezi uno. Ana a sukulu zosiyanasiyana mu bomali anali nawo pamkumanowu komwe mfundo zokhudza chitetezo cha ana pa intaneti zinatambasulidwa.
M’mawu awo, wapampando wa Board ya MACRA a Counsel Chancy Gondwe anati malo otetezeka pa intaneti amalimbikitsa anthu ogwiritsa ntchito kudziwa zinthu zosiyanasiyana. Iwo anapempha kuti intaneti tiitenge ngati nyanja yomwe imatha kukhala ndi mafunde, ndipo tipeze njira zoyenera zochepetsera komanso kuthetseratu mavutowa.
Mkulu oyang’anira ndi kumenyera ufulu wa ana, omwenso ndi mkulu wa YONECO, a McBain Mkandawire, anati pakufunika kukhala ndi anthu ochuluka opereka uphungu pankhani zokhudza nkhanza zomwe ana amakumana nazo m’masamba amchezo komanso kuwaunikira ana oterewa. Iwo anati ngakhale malamulo amagwira ntchito pa omwe achitira nkhanza ana, ochitiridwa nkhanzawo amakhala ndi mabala a nkhanzazi kwa moyo wao wonse, zomwe zimaika miyoyo yao pachiopsezo ngati salandira uphungu oyenera.
Mmodzi mwa ophunzira, Tinashe Mitengo, anayamikira mabungwe awiriwa pochititsa msonkhanowu, pakuti wathandizira kuwazindikiritsa ana pa zoyenera kuchita akachitiridwa nkhanza pa intaneti. Iye anapempha ana anzake kuti azisamala pa omwe akucheza nawo pamasamba amchezo.
